MULUNGU 1 MFUNDO ZOONADI ZENIZENI ZA BUKHU LOPATULIKA Maphunziro Owerenga Kuwulura Za Chimwemwe Ndi Mtendere Mu Chikristu Choona Duncan Heaster 2 MULUNGU MFUNDO ZOONADI ZENIZENI ZA BUKHU LOPATULIKA DUNCAN HEASTER MULUNGU 3 Bible Basics English Edition first published 1992 Chichewa Edition published 2005, reprinted 2011 Bible Basics is also available in: Afrikaans, Albanian, Amharic, Arabic, Armenian, Chinese, Estonian, Farsi, French, Georgian, Hebrew, Hungarian, Hindi, Igbo, Italian, Japanese, Kazakh, Korean, Latvian, Lithuanian, Macedonian, Mongolian, North Sotho, Polish, Portuguese, Russian, Serbo-Coat, Slovak, Spanish, Tagalog, Telugu, Turkish, Ukrainian To view available translations on-line see http://www.biblebasicsonline.com http://www.carelinks.net Published by Christadelphian Advancement Trust Company No. 3927037 Reg. Charity No. 1014615 PO Box 3034 South Croydon, Surrey CR2 0ZA ENGLAND Carelinks Publishing, PO Box 152, Menai NSW 2234 AUSTRALIA Duncan Heaster – 2005 4 MULUNGU MULUNGU 5 PHUNZIRO 1: MULUNGU 1 1.1. Mulungu Alipo 1.2 Mawonekedwe A Mulungu 1.3 Dzina La Mulungu Ndi Makhalidwe Ake 1.4 Angelo PHUNZIRO 2: MZIMU WA MULUNGU 39 2.1 Mzimu Wa Mulungu – Tanthawuzo 2.2 Mauziridwe (Mapatsidwe A Mau Ndi Mulungu) 2.3 Mphatso Za Mzimu Woyera 2.4 Kuchotsedwa Kwa Mphatso 2.5 Baibulo Lamulo Lokhalo PHUNZIRO 3 : MALONJEZANO A MULUNGU 115 3.1 Malonjezano A Mulungu Oyamba 3.2 Malonjezano A M‟munda Wa Edeni 3.3 Malonjezano Kwa Nowa 3.4 Malonjezano Kwa Abrahamu 3.5 Malonjezano Kwa Davide PHUNZIRO 4 : MULUNGU NDI IMFA 160 4.1 Uthunthu Wa Munthu 4.2 Thunthu - (Mzimu) 4.3 Mzimu Wa (Mphamvu Ya) Munthu 4.4 Κιρα Imfa Ndiko Kusapuma Komanso Kusakumbukira 4.5 Kuukanso Kwa Akufa 6 MULUNGU 4.6 Chiweruzo 4.7 Malo Olandirira Mphotho: Kumwamba Kapena Pansi? 4.8 Udindo Wathu Pamaso Pa Mulungu Yehova 4.9 Helo (Manda Kapena Kuti Dzenje) PHUNZIRO 5 : UFUMU WA MULUNGU 216 5.1 Kufotokozera Za Ufumu Wa Mulungu 5.2 Ufumu Wa Mulungu Sunakhazikitsidwe 5.3 Ufumu Wa Mulungu Kalelo 5.4 Ufumu Wa Mulungu Mtsogolomo 5.5 Chirumika PHUNZIRO 6 : MULUNGU KOMANSO CHAKWAYIPA 254 6.1 Mulungu Komanso Chakwayipa 6.2 Mdierekezi Ndi Satana 6.3 Daimoni (Mizimu Yonyansa) PHUNZIRO 7 : CHIYAMBI CHA YESU 316 7.1 Uneneri Wa Yesu M‟chipangano Chatsopano 7.2 Kubadwa Mwa Namwali 7.3 Udindo Wa Khristu Mchikonzero Cha Mulungu 7.4 “Pachiyambi Panali Mau” Yohane 1:1-3 PHUNZIRO 8 : UTHUNTHU WA YESU 352 8.1 Uthunthu Wa Yesu – Mwachidziwitso MULUNGU 7 8.2 Kusiyana Pakati Pa Mulungu Ndi Yesu Khristu 8.3 Uthunthu Wa Yesu 8.4 Umunthu Wa Yesu 8.5 Ubale Umene Ulipo Pakati Pa Mulungu Ndi Yesu PHUNZIRO 9 : NTCHITO YA YESU 371 9.1 Chigonjetso Cha Yesu 9.2 Mwazi Wa Yesu 9.3 Nsembe Ya Ife Ndi Iye Yekha 9.4 Yesu Ndiye Amatiyimira Kwa Mulungu 9.5 Yesu Potsagana Ndi Lamulo La Mose 9.6 Sabata PHUNZIRO 10 : KUBATIZIDWA MWA YESU 403 10.1 Kufunika Kwa Kukulu Kwa Ubatizo 10.2 Kodi Tingabatizidwe Bwanji 10.3 Tanthauzo La Ubatizo 10.4 Ubatizo Ndi Chipulumutso PHUNZIRO 11 : UMOYO MWA YESU 434 11.1 Chiyambi 11.2. Kudziyeretsa/ Kudzipatula 11.3 Ntchito Yoyenera Kuchita Mu Chikhristu Chathu 11.4 Ukwati 11.5 Kusonkhana Mogwirizana 8 MULUNGU PHUNZIRO 1 MZIMU WA MULUNGU MULUNGU 9 1.1.MULUNGU ALIPO “…Pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndikuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye” (A Hebri 11:6) Cholinga cha phunziro lino ndicho; kuthandiza onse omwe akufunitsitsa kusendera pafupi ndi Mulungu popeza iwo akudziwa kuti “Mulungu Alipo” choncho, sitifuna kutaya nthawi yawo powawuza kuti Mulungu alipo popeza iwowa akudziwa kale. Chimene tidzachita pano ndiye kuwonetsetsa ndi kufufuza zambiri mofananiza momwe matupi athu akuwonekera (Masalmo 139:14), tiwonanso ndi chidwi m‟mene duwa limawonekera pa chilengedwe chake, kukula kwa mlenga lenga (m‟malere), zonsezi zikuwonetsa kwaife kuzizwitsa ndi mawonekedwe ake kuti ndizoonadi, sizinalengedwe zokha ayi. Kotero, kuti munthu wina lero anene kuti kudziko kuno kulibe Mulungu, ndizofunika chikhulupiriro chozama chomwe chiyenera kuposa chikhulupiriro tiri nacho lerochi pa Yesu; chikhulupiriro chathu kawiri kawiri chikuwonetseratu kuti Mulungu alipo ndipo kupeza chikhulupiriro ichi, ndi kobvuta kwambiri. Tangoganizirani nokha kuti kusakhale Mulungu, sipangakhale tanthawuzo leni leni lomwe analengera dziko lino ndi zonse ziri m‟menemo; palibe tanthawuzo kuti kukhale usiku, masana ndi zina zotero. Chifukwa chaichi, ndizosadabwitsa kuwona kuti pafupifupi aliyense padziko lapansi amadziwa ndipo amakhulupirira kuti Mulungu alipo komanso kuti Mulunguyo amagwira ntchito yaikulu pakati paife kudzera mu zomwe zimawoneka padziko. Tikudziwanso kuti ngakhale tonse tingabvomerezane kuti kudziko kuno kuli Mulungu, timasiyana mu kazindikiridwe monga kuti Mulungu‟yo lero Mphamvu zake ziri bwanji pakati pathu, nanga malonjezano ake kwaife ndi chiyani, atanthawuzanji maka tikakhulupirira ndi kuchita chifuniro chake? Nanga ine ngati m‟modzi olengedwa ndi Iye ndingakwaniritse bwanji cholinga chake paine (yense payekha payekha)? Paulo mkalata yake kwa a Hebri 11:6 akuti; “….ayenera kukhulupirira kuti (Mulungu) alipo NDINSO 10 MULUNGU “….kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye”. Nkhani yaikulu mu Baibulo inkakhudza ana ake a ku Israeli ndipo nthawi zonse, Mulungu ankawadzudzula kuti zochita zawo ndi mabvomeredwe awo sakugwirizana ndi chikhulupiriro chawo mu malonjezano a Mulungu. Mose anawauza ana a Israeli; “….dziwani lerolino nimukumbukire m‟mitima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu m‟thambo la Kumwamba ndi dziko lapansi; Palibe wina. Muzisunga malembo ake ndi malamulo ake” (Deuteronomo 4:39,40). Munjira iyi tiyenera kuzindikira kuti ngakhale tidziwe kuti Mulungu alipo koma osachitapo kanthu, tiri chabe. Mulungu Mwini amafuna ife “tichitepo kanthu” “….muzisunga malembo ake ndi malamulo ake….kuti masiku anu achuluke.” Choncho, cholinga cha maphunziro ano mu buku lino, ndi kufuna kuphunzitsana zambiri za malamulo amene‟wa ndi m‟mene tingawasungire. Tikasanthula malembo Oyera, mu maphunziro awa, tiwonanso kuti chikhulupiriro chathu chidzakula ndikuzindikira zambiri za kukhala ndi Mulungu. “…Chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa Mau a Mulungu” (Aroma 10:17). Tikawerenganso Yesaya 43:9-12, tiwona kuti kuzindikira uneneri ndi malosero a Mulungu kudzera mwa a losi ndi aneneri ake, akutiuza kuti dzina lake lenileni la Mulungu ndi “ Chiyambire nthawi, „Ine Ndine‟ ” (Yesaya 43:13). Izi zikuphera ndemanga dzina loti; “INE NDINE YEMWE NDIRI INE” pa ndime ya Eksodo 3:14. Mtumwi Paulo pofika ku Bereya komwe ndi ku mpoto kwa dziko la Greece, analalikira za “Uthenga Wabwino” wa Mulungu. M‟malo moti anthu a chi Herene aja angokhulupirira zonse zomwe Paulo analalikira monga zikuchitikira ndi ife mu mipingo yathu lero, timva kuti anthu onse; “….analandira Mau aja ndi kufunitsitsa (ndi luntha) ndi mtima onse; nasanthula m‟malembo masiku onse, ngati zinthu zonse zinali zotero. Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira….” (Machitidwe 17:11-12). Apa tiwona kuti pali kusiyana kwakukulu pakati paife ndi anzathu awa a chi Helene. Iwo anaulandira “Uthenga wa Mulungu” (osati wa Paulo ayi), ndipo atapita ku nyumba zawo anakhala pansi nasanthulanso Mau mu Buku Lopatulika pofananiza ndi zomwe Paulo analalika ndipo ataona kuti zinali zoona, anakhulupirira nazitsata pomutsimikizira Paulo kuti analalika zoonadi. Izi MULUNGU 11 zikusiyana koposa ndi zomwe zikuwoneka masiku ano m‟matchalitchi athu komwe anthu amatembenuka mtima asanafufuze okha mu Buku Loyera ngati momwe anachitira anzathu ku Bereya pa nthawi ya Paulo. Kodi ife tiri nawo mtima wofuna kufufuza mu Baibulo tisanakhulupirire zonse zomwe zalalikidwa ndi kulembedwazi? Kufufuza koyenera ndikuzindikira bwino chomwe mwamva ndi gawo lomwe likusowa kwambiri pakati pathu. N‟chifukwa chake tiyenera kumvetsetsa bwino kuti tipindulepo mu moyo wathu wachikhristu chatsopano. Izi zingathandize kuteteza Mau a Mulungu kuti anthu ena asatisokoneze. Tikhulupirira kuti buku lino likukwaniritsa cholinga choti yense wainu aphunzire ndondomeko yoyenera pamene munthu wina aliyense akufuna kuphunzira mofufuza magawo onse a malembo Oyera. Mwaichi, mukazindikira, mudzakhulupirira ndi kuchita chifuniro chake pomvera motsata ndondomeko yake imeneyi. Pali kusiyana pakati pa kumva “Mau a Uthenga Wabwino” ndikukhala ndi chikhulupiriro mu Mau amenewa ndipo izi zawonetsedwa mu ndime zapatsidwa pansizi: -„„…Ambiri kwa Akorinto atamva anakhulupirira nabatizidwa..‟‟ (Machitidwe 18:8) -„„…amve Mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire..‟‟(Machitidwe 15:7) -„„…Kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira‟‟ (1 Akorinto 15:11) -“….Mbeu‟‟ mu “fanizo la ofesa” ndiwo Mau a Mulungu (Luka 8:11) pamene “Mbeu” ya mu “fanizo la kambeu ka mpiru” ndiye chikhulupiriro (Luka 17:6) ndipo powona kuti “Chikhulupiriro chidza pobvomereza Mau a ulaliki m‟chikhulupiriro” (Aroma 10:8-9); “woleredwa m‟mauwo achikhulupiriro ndi malangizo abwino.” (1 Timoteo 4:6) kwaiwo omwe ali ndi mitima yotseguka kuti akakhulupirire mwa Mulungu m‟mau ake (Agalatiya 2:2; A Hebri 4:2). -Yohane polemba za umoyo wa Ambuye Wathu Yesu Khristu anati; “…adziwa kuti anena zoona inunso mukakhulupirire” (Yohane 19:35) kotero tinenetsa kuti Mau a Mulungu ndiye “choonadi” (Yohane 17:17) choncho, tiyenera 12 MULUNGU kuwakhulupirira. Zoonadi Mulungu adalipo kalelo, alipo lero ndipo adzakhalapo. 1.2 MAWONEKEDWE A MULUNGU Mfundo iyi ndi imodzi yozizwitsa kwaife tikayamba kuganizira za maonekedwe a Mulungu chifukwa timamva kuti palibe yemwe anamuona Mulungu. Baibulo limatiuza kuti Mulungu amaoneka ngati momwe munthu amawonekera. Timadziwanso kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu kotero kuti ndi chifukwa chake Yesu‟yo adaonekanso
Details
-
File Typepdf
-
Upload Time-
-
Content LanguagesEnglish
-
Upload UserAnonymous/Not logged-in
-
File Pages479 Page
-
File Size-